Nathenje Broadcasting Network
Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Nathenje Broadcasting Network, Radio Station, Nathenje.
KUBWELETSA CHILUNGAMO KU MTUNDU WA ANTHU
Your Trusted Source of Verified News From Lilongwe Rural East
www.nathenjecommunityradio.blogspot.com
WhatsApp Channel: https://whatsapp.com/channel/0029Vb5oa6KKWEKytYDK3D0W
25/08/2026
MAGANIZO ANU NDI OTANI?
Dzulo chakumadzulo dziko linali lodzidzimuka kumva kuti company ya NOCMA yalipila ndalama zankhaninkhani zodutsa 700 million kwacha ku account ya anthu akuba poyesa kuti akulipila ku kampani yomwe amagwira nayo ntchito ya ku Mozambique.
Maganizo Anu ndi otani?
Kodi izi zinali zopeweka?
22/08/2026
Yanu ilipati kapena mukudikila mawa?
17/08/2026
NEWS UPDATE
Ana amene akhoza mayeso a standard 8 ndipo asankhidwa kukayamba maphunziro a sekondale mu sukulu za dela lapakati kumawa boma La Chikwawa, alandira mphatso ya zikwama ndi ndarama yokwana k100,000 aliyese.
Phungu wa derali olemekezeka a George Qoma ndiyemwe apeleke mphatsozi kutsatira lonjezo lomwe anapeleka pamene amatsazikana ndi ophunzirawa atatsala pang'ono kulemba mayeso.
A Qoma anena izi kudzera pa tsamba lawo la Facebook lero. 'Monga momwe ndinalonjezera, ndipereka chikwama komaso ndarama zokwana k100,000 Kwa mwana aliyese amene asankhidwa kukayamba maphunziro a sekondale mma sukulu a boma apamwamba."
Pothirira ndemanga mmodzi mwa kholo yemwe mwana wake asankhidwa nawo, bambo Josiah ochokera Kwa Sekeni wathokoza phunguyu kamba kosunga lonjezo lake nkukwanilisa mawu ake. Naye Yowasi Samuel, mmodzi mwa anawa wochokera mmudzi mwa Nyume walonjeza phunguyu kuti akalimbikira maphunziro ake a sekondare cholinga kuti thandizoli lipindule.
Zomwe achita a George Qoma zalimbikitsa ana ambiri pamaphunziro awo.
Olemba: Redson Dani - chikwawa
Non-governmental organisations in Mwanza have backed calls for financial assistance to be provided to prisoners upon their release, particularly to help them meet transport costs to return to their respective homes.
Martin Kadaona, Chairperson of the district’s NGO coordination body, says providing such assistance could help former inmates reintegrate into their communities. He believes the lack of transport money may force some released prisoners to engage in unlawful activities as they try to raise money for their journey home.
Kadaona has also warned that some former inmates may end up moving around the district without a clear destination, a situation he says could expose them to criminal activities.
He has therefore appealed to NGOs, faith-based organisations and other well-wishers to consider supporting the initiative, saying there is currently no organisation in Mwanza providing this kind of assistance.
The call follows an earlier appeal by Fani Master, the inmates’ leader at Mwanza Prison, who asked organisations and individuals to assist prisoners who are released with transport fares so they can safely return to their homes.
Reported by Rashid Mtumbati-Mwanza
01/08/2026
Wachiwiri kwa m'tsogoleri wa dziko lino, a Jane Ansah, wapempha anthu dziko muno kuti asakhulupirire mphekesera zoti iwo akawukira pulezidenti Peter Mutharika.
Malingana ndi kalata yomwe ofesi yake yatulutsa kudzera mwa m'neneri wake a Richard Mveriwa, a Ansah ndiwodzipereka kutumikira komanso kuthandiza a Mutharika pa masomphenya awo wotukula dziko lino.
Kalatayi yatinso wachiwiri kwa m'tsogoleri wadziko linoyu sakuyikira kumbuyo zichitochito za anthu ena zomwe zili ndi kuthekera kobweretsa chisokonezo pakayendetsedwe ka boma.
Wolemba: Dismas Puluputu
01/08/2026
Bungwe la MERA latsitsa mtengo wa mafuta a galimoto a mtundu wa diesel kuchoka pa K6, 306 kufika pa K5, 863.
Izi ndi malingana ndi kalata yomwe bungweli latulutsa kudzera mwa mkulu wake, a Lukas Kondowe.
Mafutawa atsitsidwa ndi 7 kwacha pa 100 kwacha iliyonse (7%).
Wolemba:Dismas Puluputu
31/07/2026
News update
Polisi ya boma la Nsanje, amanga mayi wazaka 23,Magret kadume,mmudzi mwa Mbeta mfumu yaikuru Malemia m'bomali, pomuganizira kuti wapha mwana wake .
Malinga ndi mneneri wa polisi bomali a Jabulani Ng'oma, mayi Margret anali oyembekezera ndipo pa 30/07/2026, mwini wa nyumba yomwe mayiwa amakhala anamva kulira Kwa khanda mnyumba mwa mayiwa ndipo poganiza kuti mkutheka nthawi yobereka mayiwa inakwana ndipo aziberekera okha, analowa mnyumba mwa mayi Margret komwe anapeza khanda la mwanalo likutuluka magazi pakhosi pomwe pamaoneka kuti panali bala lalikuru. Mwini malowa anauza anthu oyandikana nkutengera mayi ndi mwanayu ku chipatala Cha Nsanje komwe madotolo anatsikimiza kuti khandalo linali litafa kale ndipo zotsatira zachipatala atayeza thupilo laonesa kuti mwanayo wamwalira kamba kotaya magazi ochuluka.
Apolisi atalandira nkhaniyi amanga ndikutsekera mayi wa mwanayu omwe ndi Margret Kadume pa mlandu wakupha mwana ndipo kafukufuku akamaliza amutengera mayiyu kubwalo loweluza milandu.
Mayi Margret Kadume amachokera mmudzi wa Mwanavumbe mfumu yaikulu Mlolo boma la Nsanje.
Olemba: Redson Dani
28/07/2026
NEWS UPDATE
Bwalo a milandu la Nsanje, latumiza ku ndende mayi wa zaka 27 Stella siliva kuti akagwire ntchito yakalavula gaga Kwa miyezi 12,atapezeka olakwa pa mlandu otaya mwana wakhanda mchimbudzi chokumba chaka cha 2025.
Malinga ndi wapolice oimila boma pa milandu a Gladson kanyenzi wati mayi Stella siliva anali pa ubwenzi wa mtseri ndi mamuna wina ngakhale kuti anali pabanja. Ndipo pa 23/07/2025 anabereka mwana ndipo anapita kamutaya mchimbudzi chapa sukulu ya pulaimale ya Matundu m'bomali. Anthu amene anamuona mayiyo anadabwa Poona kuti alibe mwana ndipo atafufuza anapeza kuti anamugwesera mchimbudzi ndipo anthuwo anamuchosa mwanayo nkuthamangira naye ku chipatala chachikuru Cha Nsanje komwe anamwalira akulandira thandizo la chipatala.
Poyankhapo atawafunsa mu bwalo la mlandu, mayi Stella anati anavomera mlanduwu ndipo anati anapanga izi pofuna kuteteza banja lake. Ndipo anapempha bwalo kuti limumvere chisoni kamba koti akusunga ana.
Koma muchigamulo chake oweruza milandu a Haneef Ngungunde anati zomwe anachita mayizi ndizoipa zomwe zinapangisa kutaya moyo wa mwana osalakwa. A Haneef anapitiliraso kulangiza mayi Stella kuti ubwenzi wa mtseri umaika moyo wa munthu winayo pa chiopsezo chachikuru chotenga matenda opasirana pogonana. "Ngati simufuna kubereka muzigwirisa ntchito njira zolera" anamaliza motero a Haneef asanapereke chigamulo chokakhala ku ndende miyezi 12.
Mayi Stella Siliva amachokera mudzi wa Kapusi mfumu yaikuru chimombo boma la Nsanje.
Olemba: Redson Dani
27/07/2026
Police in Mangochi have arrested 29-year-old Jafali M'bwana for allegedly stabbing to death 23-year-old Sumaila Aubrey after finding him having sexual in*******se with his 38-year-old wife in their matrimonial home.
According to Mangochi Police Spokesperson, Amina Tepani Daudi, the incident happened on the night of July 25, 2026 at Stambuli Village, TA Chimwala, Mangochi District.
Daudi said the Investigations show that Aubrey was in a relationship with M'bwana’s wife and had gone to see her, thinking her husband was in Lilongwe. M'bwana returned home around midnight, forced his way into the house and found them red-handed.
He then allegedly stabbed Aubrey several times in the chest with a knife. Aubrey fled but collapsed and died a short distance away from blood loss.
She added that the body was found the next morning by a villager and reported to the village headman, who alerted Chilipa Police. A post-mortem at Chilipa Health Centre confirmed death was due to multiple stab wounds.
M'bwana has admitted to the offence and has been charged with murder under section 209 of the Penal Code. He is expected in court soon. He hails from Bonongwe Village, TA Chilipa, Mangochi.
Newsroom
19/07/2026
Mbava usiku wapitawu zathyola maofesi anayi pa sukulu ya Chikanga yomwe ili m'dera la Mfumu Yaikulu Chadza m'boma la Lilongwe, ndikuba katundu wosiyanasiyana.
Malinga ndi zomwe NBN yapeza, akubawo athyola ofesi ya mphunzitsi wamkulu, ofesi ya wachiwiri kwa mphunzitsi wamkulu, ofesi yosungira zokolola komanso ofesi yosungiramo zipangizo zina za sukuluyi.
M'modzi mwa ogwira ntchito pa sukulupo, yemwe wati tisamutchule dzina, wati zikuoneka kuti akubawo anagwiritsa ntchito zida zolimba pothyola maloko a maofesi onsewo ndipo kufikira nthawi ino, katundu yemwe watsimikiziridwa kuti wabedwa ndi matumba a chimanga ndi mtedza.
Komabe, akuluakulu a sukuluyi ati kuchuluka kwa katundu yemwe wabedwa kudzadziwika akamaliza kufufuza ndi kuwerengera zinthu zonse zomwe zinali m'maofesiwo.
Izi zadabwitsa anthu ambiri okhala m'derali chifukwa sukuluyi ili ndi mlonda amene amalondera usiku, ndipo mlondayo akuti anabwera kuntchito monga mwa nthawi zonse.
Pakadali pano apolisi sadayankhulepo pa nkhaniyi, pomwe kafukufuku wokhudza omwe achita umbavawu ukupitirira.
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Address
Nathenje
Alerts
Be the first to know and let us send you an email when Nathenje Broadcasting Network posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.